6
Milandu Pakati pa Anthu Okhulupirira
Pamene wina wa inu ali ndi mlandu ndi mnzake, nʼchifukwa chiyani amatengera nkhaniyo kwa anthu akunja kuti akawaweruze mʼmalo mopita nayo kwa oyera mtima? Kodi inu simukudziwa kuti anthu a Mulungu adzaweruza dziko lapansi? Ndipo ngati inu mungaweruze dziko lapansi, kodi sindinu oyenera kuweruza milandu ingʼonoyingʼono? Kodi simukudziwa kuti mudzaweruza angelo? Nanga bwanji zinthu za mʼmoyo uno! Nʼchifukwa chake, ngati pali milandu pa zinthu zotere, sankhani anthu ena kuti akhale oweruza ngakhale alibe udindo mu mpingo. Ndikunena izi kuti ndikuchititseni manyazi. Moti nʼkutheka kuti pakati panu palibe wina wanzeru zokwanira kuti aziweruza mlandu pakati pa Akhristu? Koma mʼmalo mwake mʼbale atengera ku bwalo la mlandu mʼbale mnzake kukaweruzidwa. Zonsezi pamaso pa akunja!
Chokha choti mwakasumirana chikuonetseratu kuti mwagonjetsedwa kale. Bwanji osangolola kuti ena akulakwireni? Bwanji osangolola kuti ena akubereni? Mʼmalo mwake, inuyo ndiye mumabera ena ndi kuwalakwira, ndipo mumachita izi kwa abale anu. Kodi simukudziwa kuti munthu woyipa sadzalowa mu ufumu wa Mulungu? Musanyengedwe: achigololo, kapena opembedza mafano, kapena achiwerewere, kapena amuna adama, kapena ogonana ndi amuna okhaokha; 10 kapena akuba, kapena aumbombo, kapena oledzera, kapena achipongwe, kapena opeza ndalama mwachinyengo sadzalowa mu ufumu wa Mulungu. 11 Ndipo umu ndi mmene ena mwa inu munalili. Koma munatsukidwa, munayeretsedwa, munalungamitsidwa mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu ndi Mzimu wa Mulungu wathu.
Chigololo
12 Inu mumati, “Ine ndili ndi ufulu wochita chilichonse.” Komatu si zonse zimene nʼzothandiza. “Ndili ndi ufulu wochita chilichonse.” Koma sindidzagonjetsedwa ndi chilichonse. 13 Inu mumati, “Chakudya, kwake nʼkulowa mʼmimba ndipo mimba ntchito yake nʼkulandira chakudyacho.” Koma Mulungu adzawononga zonsezi. Thupi silochitira chigololo, koma la Ambuye, ndipo Ambuye ndiye mwini thupilo. 14 Mwamphamvu zake Mulungu anaukitsa Ambuye kwa akufa, ndipo ifenso adzatiukitsa. 15 Kodi simukudziwa kuti matupi anuwo ndi ziwalo za Khristu mwini? Kodi tsono ndingatenge ziwalo za Khristu nʼkuzisandutsa ziwalo za mkazi wadama? Zosatheka! 16 Kodi simukudziwa kuti amene amadzipereka kwa mkazi wadama, iyeyo ndi mkaziyo amasanduka thupi limodzi? Paja kunalembedwa kuti, “Awiriwo adzakhala thupi limodzi.” 17 Koma amene amadzipereka kwa Ambuye, iyeyo ndi Ambuye amakhala mzimu umodzi.
18 Thawani dama. Machimo onse amene munthu amachita amakhala kunja kwa thupi lake, koma amene amachita machimo okhudza chigololo, amachimwira thupi lake lomwe. 19 Kodi simukudziwa kuti thupi lanu ndi Nyumba ya Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene mwalandira kuchokera kwa Mulungu? Inu simuli panokha ayi. 20 Ndinu ochita kugulidwa. Nʼchifukwa chake lemekezani Mulungu mʼthupi lanu.